sexta-feira, 18 de maio de 2018

PORTRAIT OF A DICTATOR: The Rise and Fall Of Lazarus Chakwera

PORTRAIT OF A DICTATOR: The Rise and Fall Of Lazarus Chakwera

KUFUNIKA KWA KUSINTHA ZINTHU
NDI KUYAMBANSO MOYO WATSOPANO M’MALAWI
Kalata ya Aepiskopi Achikatolika m’Malawi Yotsindikizidwa pa: 29 April 2018
Bungwe la Aepiskopi Achikatolika m’Malawi (ECM)
Kalata Ya Aepiskopi Achikatolika m’Malawi (ECM)
Malonje
Abale ndi Alongo mwa Khristu, lero pa Lamulungu la 5 la Pasaka, tikukulonjerani nonse pamene tikukondwerera kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu ku mtundu wa anthu kudzera m’kuuka kwa akufa kwa
Ambuye athu Yesu Khristu. Mulimbikitsidwe m’chikhulupiriro chanu, mukule m’chikondi cha Mulungu, khalani ndi chiyembekezo chosagwedezeka, mudalitsidwe ndi mphamvu za Mzimu Woyera ndipo mukhale ndi chimwemwe ndi mtendere wa Khristu wouka kwa akufa.
Mau Oyambirira
Ife, Aepiskopi anu, pozindikira udindo wathu wakumva “chimwemwe ndi chiyembekezo, chisoni ndi nkhawa za anthu a m’nthawi yathu ino, makamaka nkhawa za anthu osauka kapena osautsidwa mwanjira zosiyanasiyana” (Gaudium et Spes no. 1) kukhala zathu, tili okhudzidwa ndi okhumudwa kuona kuti ufulu wademokalase womwe tidaawupeza movutikira m’dziko lathu lino, sudabereke zipatso zomwe tinkayembekezera. Tikuona ndi kumva chisoni chachikulu kuti anthu ambiri m’dziko lathu lino la Malawi, akukhala mu umphawi wadzaoneni, ambiri ndi osaphunzira, akuzunzika ndi matenda osiyanasiyana, njala, ndi kaganizidwe kopotoka kamene kakuchititsa anthu kukhala ndi makhalidwe osayenera ndi onyansa pakati pathu. Pambuyo pa zaka 54 tikudzilamulira, Amalawi sitinafikebe ndipo sitinakwaniritse zomwe tinkalakalaka kukhala nazo. Tili ndi zinthu zambiri zabwino zomwe Mulungu adatidalitsa nazo monga mtima umene anthu ali nao wogwira ntchito modzipereka, Nyanja yomwe ndi yachitatu kukula kwake mu Africa, nthaka yachonde, mapiri aakulu opatsa chidwi, zachilengedwe zochuluka ndiponso mphatso ya mtengo wapatali ya mtendere yomwe dziko lidakhala nawo chilandilireni ufulu wodzilamulira. Ngakhale dziko lathu lidadalitsidwa motere, Malawi ndi limodzi mwa maiko osaukitsitsa m’dziko lapansi. Izitu zitanthauza kuti pakufunika kuti tonse tiganize ndi kusinkhasinkha mozama. M’kalata ino, ife Aepiskopi anu, tayesa kupereka maganizo pa mfundo zoyenera kuti tiziganizire mozama ngati tifunadi kuti tikwanitse kukhala Fuko la umunthu, lotukuka ndi lodziimira palokha ngati ufulu wa demokalase umene tidasankha ndi kuupeza zaka 25 zapitazo ukuyenera kubereka zipatso ndi kukhala watanthauzo.
MUTU 1
KUFUNIKA KWA KUSINTHA ZINTHU M’MALAWI
Ife, Aepiskopi anu, pokwaniritsa udindo womwe tidalandira wofalitsa
Mthenga Wabwino wa Ambuye, “pa nthawi imene anthu akuufuna angakhalenso pamene sakuufuna”, (2 Timoteo 4: 2), tikufuna kukumbutsa Mtundu wa Malawi kuti pali zinthu zina zimene sizikuyenda bwino pakati pathu zofunika kuzikonza mwansanga. Tikuganiza kuti, Malawi ngati dziko, tisoweka kusintha pa kayendetsedwe ka dziko lathu ngati tikufunadi kuti zinthu zisinthe. Apa tikutanthauza kuti, tiyenera kusintha kotheratu pakachitidwe ka zinthu ndi kayendetsedwe ka dziko m’malo mongochita zinthu mwachizolowezi. Izi zitanthauza kusintha kaonedwe ndi kaganizidwe kathu komwe kangatithandize kuti pakati pathu pakhale kufunirana zabwino ndi chilungamo kwa anthu onse. M’munsimu, tiwona ena mwa magawo kapena madera amene tiyenera kusintha kotheratu pa kaganizidwe ndi kaonedwe ka zinthu ka Amalawi onse.
1.1 Ufulu Wademokalase Kuno Ku Malawi
Pamene dziko la Malawi likukondwerera kuti papita zaka 25 chiyambireni ufulu wademokalase, ndi kofunika kusinkhasinkha mozama za zomwe zakwaniritsidwa potsata ndondomeko ya demokalase yoyendetsera dziko lathu. Tikuyenera kudzifunsa ngati demokalase imene tidasankha yakwaniritsadi kutukula miyoyo ya Amalawi kapena ili ngati nkhambakamwa chabe pamene anthu ochepa okha amene ali ndi udindo ndi ulamuliro ndi amene akusangalala ndi chuma cha dziko la Malawi pamene kwinaku anthu ochuluka ali mu ulombo ndi umphawi wosasimbika. Amalawi, tisamadzinamize kuti zinthu zili bwino.
1.2 Momwe Zinthu Zinaliri Tisanafike Chaka cha 1993
Zaka zimene dziko la Malawi linali lisanalandire ufulu wademokalase, zinali zaka za mdima ndi za ukapolo. Izi ndi zomwe Kalata ya Aepiskopi ya 1992 yotchedwa ‘Kukhala Moyo M’chikhulupiriro Chathu’ idafotokoza poyera mosabisa Chichewa. Amalawi ambiri adaalibe mwai wotenga nawo mbali pakayendetsedwe ka dziko lao. Kulankhula zakukhosi mwaufulu kunali kosaloledwa ndipo kusiyana kwa maganizo kunkaponderezedwa. Malamulo sankatsatidwa moyenera ndipo chilungamo chinkangokomera anthu ochepa okha. Panalibe mwai wokambirana pa mfundo zoyendetsera dziko ndi zinthu zina zofunikira pakati pa anthu. Umembala wa chipani unali wokakamiza ndipo maudindo pa nthawiyo anali ongolozedwa osati osankhidwa ndi anthu. Maudindo ankaperekedwa mokondera ndi mosankhana mitundu. Komatu, ngakhale m’kati mwa ulamuliro wamphamvu wosapereka mpata kwa wina aliyense wa maganizo osiyana, ganizo lotufuna udindo silingalepheretsedwe ngakhale munthu apanikizidwe motani, zingathe kudzetsa mavuto aakulu pandale ndi pamoyo wa anthu watsiku ndi tsiku. Potopa ndi njira ya kayendetsedwe ka dziko, yomwe idaali yopindulira anthu ochepa okha, Amalawi, pa 14 June, 1993 adaganiza ndi mtima umodzi ndiponso mwamphamvu kukana ulamuliro wa chipani chimodzi ndi kusankha ulamuliro wademokalase wa zipani zambiri. Motero, nkofunika kuti tisinkhesinkhe mozama za zomwe zachitika mu ulamuliro wa zipani zambiri m’dziko lathu lino.
1.3 Ufulu Wademokalase M’zipani Zandale
Udindo wa zipani zandale mu ulamuliro wa zipani zambiri monga momwe zinthu ziliri kwathu kuno ngwaukulu ndi wofunika kwambiri. Kawirikawiri anthu ofuna kuima nawo pa zisankho amachokera m’zipani zandale zomwe zimawapatsa mwai woti anthu awavotere. Kudzera mu mfundo za zipani (manifesito) zipani zandale zimakonza ndondomeko za zomwe zikufuna kudzakwaniritsa zitatenga utsogoleri. Poyang’anira zimenezi, chipani chikapambana chimayembekezereka kukwaniritsa zomwe chinali kulonjeza anthu zopezeka m’manifesito ake. Nazonso zipani zotsutsa zili ndi udindo waukulu wopereka maganizo ndi mfundo zina zosiyana zothandiza kuti chipani chomwe chikulamulira chichite bwino koposa komanso kuti asatayilire ndi kumayendetsa dziko monga momwe angafunire. Indedi, ndi kudzera m’zipani zomwe Amalawi amasankha zomwe zimayenera kupereka mwai kwa mamembala ake kulankhula ndi kukwaniritsa maufulu ao mogwirizana ndi Malamulo oyendetsera dziko (Konstitushoni).
Monga m’mene tafotokozera pamwambapa, ndi chachidziwikire kuti kuchita bwino pa nkhani ya ufulu wathu wademokalase kumatsamira ndi kudalira m’mene ufulu wademokalase udamvetsedwera ndipo m’menenso ukuyendera m’zipani zosiyanasiyana. Masomphenya athu ndi zomwe tinkalakalaka pofuna kukhala ndi ufulu wademokalase wopindulira Amalawi sungakwaniritsidwe ngati m’kati mwa zipani zandale - kaya ndi chipani cholamula ngakhalenso zipani zotsutsa mulibe ufulu wademokalase. Ufulu wademokalase utanthauza kuti mamembala am’chipani azimva kuti chipanicho ndi chao ndipo ndi iwowo ali ndi mphamvu zochiyendetsera.
Mamembala onse am’zipani ndiye amene amayenera kukhala ndi mphamvu ndi kumawongolera atsogoleri ao kuti ulamuliro m’zipani ukhale wokomera anthu onse potsata constitution yao osati ulamuliro wongokomera atsogoleri okha ai.
Koma ndi zomvetsa chisoni ndiponso zokhumudwitsa kuti chiyambireni cha ufulu wademokalase m’chaka cha 1993, zipani zambiri zandale mwinanso tingoti zipani zonse kuno ku Malawi, zalephera kukwaniritsa ufulu wademokalase m’katikati mwa m’zipani zaozo. Monga tidaafotokozera m’Kalata yathu ya 2008 yotchedwa ‘Kutenga Udindo wa Tsogolo Lathu ndi Kuwerenga Zizindikiro za Nthawi’, pali zitsanzo zambiri za momwe ufulu wademokalase ukulepherera kukwaniritsidwira m’zipani zandale ndipo zina ndi zotsatirazi:
• Mfundo zazikuluzikulu zimapangidwa ndi mtsogoleri wachipani yekha ndipo nthawi zina amangofunsa maganizo a anthu okhawo omwe ndi anzake, kaya atidyenao mwinanso maganizo a anzake ochokera ku mtundu wake;
• Kulephera kukambirana poyera za zipani zoyenera kukhala nazo pa mgwirizano pa nthawi ya zisankho, kuchita zinthu m’chibisibisi posankha munthu wodzaimilira chipani ngati pulezidenti ndi wachiwiri wake;
• Maudindo ambiri am’zipani amasankhidwa ndi mtsogoleri wachipani yekha m’malo mochita masankho pa msonkhano waukulu wa chipani – konveshoni;
• Misonkhano yaikulu ya zipani – konveshoni – sichitika kawirikawiri ndipo ikati ichitike imangokhala yachiphamaso chabe mfundo zitapangidwa kale mopanda kukambirana mokwanira;
• Zotsatira za chisankho zimakhala zitakonzedwa kale ndipo msonkhanowo umangokhala ngati kumnyatika anthu m’maso chabe;
• Chisankho cha Khansala kapena Phungu wa ku Nyumba ya
Malamulo kawirikawiri sichichitika mwaufulu ndi mwachilungamo;
• Akuluakulu a zipani ndi anzao ogwirizana nawo amakonderedwa, chinthu chomwe chimakhumudwitsa mamembala ena omwe pambuyo pake amachoka nkukalowa zipani zina;
• Mamembala amene amakhala ndi maganizo ndi mfundo zosiyana ndi zotsutsana ndi atsogoleri awo amachotsedwa m’chipani ndipo amatengedwa ngati anthu ogalukira ndi kumatchedwa maina osiyanasiyana amnyozo;
• Zipani zamphamvu zili ndi chizolowezi chogula mamembala a zipani zina ndi kumawasonyeza pa misonkano yandale ndi cholinga chofuna kugwetsa mphwayi zipani zinazo;
• Ntchito zachitukuko zina zimachitika m’madera momwe muli anthu okhalira kumbuyo kwa chipani cholamula;
• Kusowa kwa mfundo zopitirizira zitukuko zosiyanasiyana m’dziko chifukwa chakuti chipani chilichonse chimene chalowa m’boma chimabwera ndi maganizo akeake;
• Kuchepa kapena kuperewera kwa zosowekera za anthu zomwe boma limayenera kupereka kwa nzika zonse za m’dziko ndipo ndi mamembala okha am’zipani zolamula omwe amakhala ndi mwai wopeza zoyenerera pa moyo wao;
• Ndi zosadabwitsa tsono kuona kuti mamembala otchuka amakanidwa ku chipani chao koma akayima ngati independenti, amapambana.
Ndizomvetsa chisoni kuti izi ndi zimene zikuchitika m’zipani zonse zandale m’dziko lathu lino. Pamene tikukondwerera zaka 25 za ufulu wademokalase, tivomereze kuti kulepherera kwathu m’zipani sikudatithandize mokwanira monga m’mene tinkafunira pamene tinkasankha ulamuliro woterewu. Sitingavomereze atsogoleri a zipani zandale amene amapondereza ufulu wademokalase m’zipani zao ndi kumaopseza anzao nkumayembekezera kuti akadzalowa m’boma adzasintha. Kugwadira ndi kuombera m’manja atsogoleri komwe kwafala m’zipani zandale kukunka kukulirakulira. Pa zinthu ngati izi, tikuyenera kusinthiratu kaganizidwe ndi machitidwe athu.
Motero, tikupempha atsogoleri a zipani zonse m’dziko lino kuti asinthe ndi kuyamba kulimbikitsa ufulu weniweni wademokalase kuyambira m’zipani zao. Ndi mwanjira imeneyi pamene tingathe kunena kuti ku Malawi kuli ufulu wademokalase yeniyeni.
1.4 Momwe Nzika Zimaganizira za Ufulu Wademokalase
M’Malawi Kuti ntchito yokhazikitsa demokalase yeniyeni itheke m’dziko lathu la Malawi, ikudalira m’mene nzika zimamvetsera tanthauzo ndi kutenga nawo mbali polimbikitsa ufulu wademokalase. Amalawi ambiri amafunitsitsa ulamuliro wa ufulu wademokalase. Iwo amadziwa ubwino wa demokalase chifukwa nzika zimakhala ndi ufulu wolankhula zakukhosi, ufulu wopembedza, ufulu wa mabungwe, ufulu wa ofalitsa nkhani, ndi maufulu ena otero.
Ngakhale zinthu zili chonchi, anthu ambiri masiku ano sakhulupirira atsogoleri andale omwe amachita zinthu zokomera iwo okha nkumaganiza kuti akuthandiza anthu. Izi zili chonchi chifukwa cha katangale amene amalepheretsa atsogoleri athu kupereka zosowa za anthu pa moyo wao monga thandizo la zaumoyo, magetsi - omwenso amazimazima kumene alipo, maphunziro oyenera ndiponso kulekerera kuti anthu ena m’dziko lino akhale olemera kwambiri pamene ena ali mu umphawi wadzaoneni ndipo alibe mwai woti angatukuke pa moyo wao. Pa chifukwa ichi, Amalawi ambiri adayamba kuyamikira zachitukuko zamphamvu zomwe zinkachitika mu nthawi ya ulamuliro wa chipani chimodzi. Mtima womacheukira ndi kumayamikira za m’mbuyo nthawi yomwe tidaali mu mdima, ndi uthenga waukulu woti ife tonse titolepo phunziro lakuti zinthu sizili bwino m’dziko lathu lino masiku ano.
Kuno ku Malawi, tili ndi mtima ndiponso chizolowezi cholemekeza anthu otitsogolera mobzola muyeso. Izi zimaoneka m’mene Prezidenti tidampatsira mphamvu zambiri zoti atha kusankha m’maudindo osiyanasiyana m’boma anthu amene iyeyo akuwafuna omwe nthawi zambiri amakhala akwao kapena anzake omwe cholinga chao nkudya nao. Izi zimapereka chithunzithunzi chakuti boma ntchito yake nkupindulira anthu okhawo amene amadziwana ndi akuluakulu. Apatu zikuonetseratu poyera kuti palibe ndondomeko zabwino zoonetsetsa kuti Boma likukwaniritsa udindo wake mokomera aliyense ndipo kuti nthambi zonse zitatu za Boma zili ndi ufulu wokwaniritsa udindo wake mopanda wina kulowererapo.
Nkofunika kuti atsogoleri pamzere uliwonse aone ndi kuunikanso udindo wao woyendetsera Boma potsata Malamulo a dziko la Malawi mopindulira nzika za dziko lathu. China ndi chakuti, atsogoleri amakhala pa maudindo chifukwa cha anthu. Ufulu wademokalase sungakhale ndi tanthauzo ngati sugwiritsidwa ntchito pofuna kutukula ndi kupezera anthu zosowa zao. Kukhumudwa kwa nzika chifukwa cha momwe atsogoleri akuyendetsera dziko, makamaka poona kuti ndi anthu ochepa okha amene akupindula, zikupereka chiopsezo ku demokalase yathu yomwe siinakhwime. Atsogoleri a zipani zandale ndi anthu ogwira ntchito m’Boma akuyenera kugwira ntchito mosiyana ndi m’mene akuchitira tsopano kuti Amalawi ayambenso kuwakhulupirira. Malinga ndi mau a Papa Fransisko, “Ndale zabwino ndi zosoweka pakati pa anthu chifukwa ndi zomwe zingathe kukonza ndi kusintha zinthu, zothandiza kuwongolera mabungwe ndi makampani ndiponso kulimbikitsa makhalidwe ndi machitidwe abwino ndi kuthetsa mtima woponderezana” (Laudato Si` no. 181). Atsogoleri ndiponso nzika zonse tikuyenera kuzindikira kuti demokalase yoona singolimbikitsa maufulu ndi kupatsa anthu mwai chabe, komanso kuti anthu akhale ndi kutenga udindo pa chinthu chilichonse chimene achita. Ndipo malinga ndi mau a Papa Benedicto, “Ndi pokhapo pamene tikhala ndi makhalidwe oyenera, molemekezana ndi mokondana wina ndi mnzake, pamene demokalase ingapite patsogolo” (Pope Benedict XVI, Solemnity of the Immaculate Conception of the Blessed Virgin Mary, Thursday, 8 December 2005).
Ngati dziko, tikhale ndi mtima wolimbikitsa magulu onse oona momwe Boma likugwirira ntchito potsatira Malamulo Oyendetsera dziko lino ndi kuwonetsetsa kuti nthambi iliyonse ya Boma ikugwira ntchito mosalowerera ntchito za nthambi zina. Izi zidzathandiza kuti Boma likwaniritse zomwe anthu adalisankhira. Anthu angathe kuyambanso kukhulupirira Boma ngati nthambi zothandiza kukwaniritsa malamulo zipatsidwa mwai wogwira ntchito mwaufulu, mosajejemetsedwa ndi mwaukadaulo. Amalawi ambiri amaganiza kuti nthambi zothandiza kukwaniritsa malamulo zilibe mphamvu zoti nkulimbanirana ndi anthu achuma amene ali ndi maudindo akuluakulu. Izi ndi zimene zimadzetsa mtima wosatsata malamulo ndi kulemekeza mabungwe a Boma.
MUTU2.
NTCHITO ZOTHANDIZA ANTHU M’DZIKO
2.1 Ntchito Zaumoyo
Ntchito zaumoyo sizili bwino ai. Mavuto amene ali m’zipatala kuno ku Malawi ndi monga kusowa kapena kuchepa kwa ogwira ntchito zaumoyo ophunzitsidwa bwino, kusowa kwa mankhwala ofunikira ndi kusowa kwa zipangizo. Mavutowa amakulirakulira chifukwa cha kuchepa kwa madokotala, kusowa kwa ukhondo, ndi kuperewera kwa zipangizo zosowekera.
Mavuto a m’zipatala zikuluzikulu (Central Hospitals) adafika poipa chifukwa cha akamberembere amene amasowetsa ndi kuba mankhwala nkumakawagulitsa pofuna ubwino wa iwo okha. Magulu amtunduwu omwe ali ndi luso lakuba akukhudza ena mwa antchito a zachitetezo, madokotala amene, anthu ena amene ali ndi zipatala zaozao ndiponso anthu ena ogwira ntchito m’Boma omwe amatengerapo mwai wa kupezeka kwa mankhwala m’zipatalazi. Mndandanda wa anthu akuba mankhwala ukukhudza anthu osiyanasiyana ndi ndondomeko yake ya kagulidwe ka mankhwalawa. Izi zimachititsa kuti ngakhale mankhwala otha ntchito agulitsidwe.
Ndi mchitidwe wakatangale womwe udakhazikika pakati pathu, ngakhalenso m’ntchito zaumoyo, sitingayembekeze kuti zinthu nkuyenda bwino. M’mau ake Papa Fransisko adaati; “Katangale ndi mliri ndiponso ndi khwekhwe lokhikha anthu pakhosi (Pope Francis, 12 July 2015). Anthu odwala pamodzi ndi owadwazika ao, amaumirizidwa kuti azichita kupempha chithandizo cha mankhwala. Chilichonse, kuyambira kukumana ndi dokotala, kujambulidwa, kupeza bedi ngakhalenso kulandira nsima ya mgaiwa ndi kabiki wofwafwaza kapena nyemba, ndi zinthu zokhalira anthu ochepa okha omwe amayenera kupereka ndalama yomwe amaipeza movutikira. Izitu zili choncho ngakhale zinthuzi zimayenera kukhala zaulere ndipo zonsezi zimachitika akuluakulu ali chete akungoyang’ana.
2.2 Za Maphunziro ndi Midadada Yophunziriramo
Ntchito zamaphunziro ndi zolowa pansi kwambiri ndipo zimakumana ndi zokhoma zambiri. Ena mwa mavutowo ndi odziwika kale monga:
• kuchuluka kwa ophunzira poyerekeza ndi chiwerengero cha aphunzitsi;
• kuchepa kwa aphunzitsi amene adasulidwa bwino pa ntchito yao;
• kuchepa kwa malipiro a aphunzitsi;
• kusowa kwa ndondomeko yabwino yogwirira ntchito yao;
• kusowa kapena kuchepa kwa midadada yophunziriramo;
• kusowa kwa zipangizo zophunzirira;
• kusinthasintha kwa ndondomeko ya maphunziro ndi kusakonzekera bwino ndi mokwanira.
Monga tidaanena m’Kalata yathu ya m’chaka cha 2016, anthu amene ali ndi udindo mu dipatimenti ya maphunziro akuyenera kuganizira ndi kuikapo ndalama zokwanira ngati dziko lathu la Malawi liyenera kutukuka ndi kupita patsogolo pa nkhani ya maphunziro (Chifundo cha Mulungu Ngati Njira Yachiyembekezo No. 2.9)
2.3 Ulimi ndi Kukhala Chakudya Chokwanira
Chuma cha dziko la Malawi chimadalira kwambiri pa ntchito za ulimi. Gawo limeneli lili ndi kuthekera kotukula ntchito za m’mafakitale. Ngakhale zili choncho, kuthekera kumeneku sikutheka chifukwa cha zinthu zingapo monga kudalira ulimi wamvula, kusowa kwa ndondomeko zabwino zokololera madzi, kusintha kwa nyengo, kusachita ulimi wakasinthasintha wa mbeu, kukwera mtengo kwa zipangizo za ulimi makamaka kwa alimi osauka, mchitidwe wa katangale pa nkhani ya zipangizo zaulimi zotsika mtengo (FISP) ndiponso kusowa kwa misika yodalirika yoti alimi nkumakagulitsako mbeu zao makamaka kumadera akumidzi. Ufulu wokhala ndi chakudya chokwanira ndi ufulu wa munthu aliyense. Dziko la Malawi likusowa kukhala ndi ndondomeko ndi njira zothandiza kuti lizikhala ndi chakudya chokwanira. Payenera kukhala misika komwe alimi angathe kumakagulitsako mbeu zao mosavuta kuti thukuta lomwe adakhetsa liwapindulire. Monga tidaafotokoza m’Kalata yathu ya 2016, nkofunika kuti pakhale kusintha pakayendetsedwe ka ntchito ya zipangizo zaulimi zotsika mtengo kapena payenera kukhala njira yosiyira ndondomekoyi (Chifundo cha Mulungu Ngati Njira Yachiyembekezo No. 2.10).
2.4 Zomangamanga
M’nthawi ino ya ulamuliro wa zipani zambiri, pachitika zinthu zambiri zothandiza kusintha chithunzi kapena nkhope ya dziko la Malawi kudzera m’zomangamanga monga nyumba ndi miseu ndi zina zotero. Koma kawirikawiri, chitukuko cha mtunduwu sichiyenda bwino chifukwa cha zofuna ndi zolinga za anthu ena, kulowetsamo ndale, katangale, kusowa mapulani abwino ndi kuchepa kwa zipangizo zogwirira ntchito. Pali ntchito zambiri zachitukuko zimene zikulephera kutsirizika ndipo zina zidutsa nthawi imene zidayenera kukhala zitatha. Zotsatira zake, pamasoweka ndalama zina zoonjezera kuti ntchitozo zitsirizike ndipo zambiri zimakhala zosalimba chifukwa chakuti ntchitozo zidaaperedwa kwa amene alibe ukadaulo womanga.
Mwa zonsezi, vuto lalikulu ndi katangale. “Chilonda chimeneni – chotchedwa katangalechi – ndi tchimo lalikulu limene Mulungu sakondwera nalo chifukwa limapereka chiopsezo ku chitukuko cha munthu pakati pathu” (Pope Francis, The Face of Mercy, no. 19). M’dziko la Malawi, katangale adakhazikika m’madipatimenti ndi mwa anthu ogula katundu. Vutoli likukula chifukwa nawonso andale amalowereramo pofuna kuti adzilemeretse okha. Izi zachititsa kuti ntchito zomangamanga zichuluke zomwe zimapindulira anthu ochepa amene amakhala pa mgwirizano wochita za chinyengo pakagulidwe ka katundu pomwe anthu ochuluka akukhala mozunzika.
Tikuyenera kudzifunsa kuti kodi chofunikira kwambiri pa zomangamanga ndi chiani kuti titukule dziko lathu? Chifukwatu nthawi zina, zimaoneka ngati kuti ndalama zimene timakongola zomwe zikadatha kugwiritsidwa ntchito mopindulira anthu monga kulola madzi, ulimi wamthilira, kugwiritsa ntchito mphamvu za dzuwa, zimalowa ku ntchito zina zomwe zidzatenga zaka zambiri kuti tibwezere ngongoleyo. Potero, tikusenzetsa mibadwo yamtsogolo ndi goli la ngongole yovuta kubweza yomwe ikadatha kugwiritsidwa ntchito pa zinthu zaphindu.
2.5 Nkhani ya Munthu Womelera ndi Lazaro ku Malawi
Nkulakwira anthu kumaganiza kuti pambuyo pa zaka 54 za ufulu wodzilamulira, moyo wa Amalawi udatukuka. Kunena zoona, zinthu siziliri choncho. Anthu ambiri alibe madzi abwino akumwa, alibe zipangizo zothandiza kuti akhale aukhondo, alibe magetsi ndipo m’madera mwao mulibe miseu yodalirika. Izinso zikuwoneka m’matawuni ndi m’mizinda ikuluikulu chifukwa chosowa mapulani abwino a zachitukuko. Zikuonekanso kuti andale amalowererapo ndiponso kuli katangale wosaneneka komanso palibe ndondomeko yabwino yoyendetsera chuma. Ndi zachidziwikire kuti Amalawi ambiri akukhala m’moyo waumphawi ndi womvetsa chisoni pamene atsogoleri amene adasankhidwa ndi anthu osauka omwewo, akukhala m’moyo wachiwofowofo m’nyumba zapamwamba. Nkhani ya munthu wolemera ndi Lazaro yomwe timaiwerenga m’Baibulo ikuchitikanso pakati pathu (cf. Lk 16: 19 – 31). Pomwe chiwerengero cha anthu chikunka chichulukirachulukira modetsa nkhawa koma kwinaku chuma chisakuyenda bwino, zimenezi zingathe kudzetsa chipwirikiti ngati sitichitapo kanthu. Nchifukwa chake tikupempha kuti pakhale kusintha pa kaonedwe ndi kaganizidwe kathu pogwira ntchito zathu zinthuzi zisanafike poipa.
Mwina vuto lalikulu la Boma ndi dziko lathu ndi kusowa kwa ndondomeko ya m’mene tingachepetsere kusiyana pakati pa anthu olemera ndi anthu osauka. Papa John Paul II adaalemba kuti; “Tchimo lalikulu m’dziko lapansi ndi lakuti, ndi ochepa amene ali ndi zinthu zambiri pamene anthu amene ali ndi zochepa kapena amene alibiretu kanthu ndiwo ochuluka” (Sollicitudo Rei Socialis, no. 28). Papa Fransisko satopa kutikumbutsa za kusiyana kosayenera kwa pakati pa anthu amene ali ndi chuma chambirimbiri ndi amene alibiretu kanthu. Ngakhale mabungwe enanso akuluakulu monga United Nations amavomereza kuti kusiyana kosayenera kumeneku ndi tchimo lalikulu m’zaka zamakono. (Mutha kuona uthenga wa Mlembi Wamkulu wa United Nations, Antonio Guterres, 1st February 2017). Kusiyana kwa anthu amene ali ndi zambiri ndi amene alibiretu kanthu nkosachita kufunsa pakati pathu ife Amalawi ndipo kukunka kuukulirakulira. Zitsanzo zoti tithe kuziganizira ndi zambiri monga anthu amaudindo akuluakulu amene amakhala ndi mwai wogula galimoto zodula koma osalipira msonkho, kukhala m’nyumba za lendi zaulere, maphunziro aulere a ana awo, thandizo laulere ku chipatala, ma alawansi aphwamwamwa ndi zina zambiri zomwe zimalipiridwa ndi misonkho ya anthu osauka.
2.6 Kuwonongeka Kwa Chilengwe
Nkhani ina yofunikira kuiganiziranso ndi ya kuwongeka kwa chilengedwe. Kawirikawiri chilengedwe chimaonongeka pofuna kulemeletsa anthu olemera kale. Chitsanzo ndi monga kuwonongeka kwa nkhalango ya Chikangawa. Papa Fransisko adafotokoanso za kulumikizana kwa kusauka kwa anthu osauka kale ndi kuwonongeka kwa chilengedwe. “Poononga chilengedwe, munthu amaonongekera limodzi ndi chilengedwecho….kunena zoona, kuwongeka kwa chilengedwe ndi kwa anthu kumakhudza kwambiri anthu amene ali osauka kale” (Laudato si`, no. 48) Nayenso Papa Benedicto akutsindika za kulumikizana kwa chisamaliro cha chilengedwe ndi moyo wabwino wa anthu pamene adaati; “Kusamalira chilengedwe, kuchita chitukuko chokhazikika makamaka poganiziranso za kusintha kwa nyengo ndi zinthu zimene mtundu wa anthu unayenera kuziganizira mozama”. (Pope Benedict XVI, Letter to the Ecumenical Patriach of Constantinople on the Occasion of the Seventh Symposium of the Religion Science and the Environment Movement, September 1, 2007). Kuwonongedwa kwa chilengedwe kuno Malawi kukuoneka poyera ndi mmene nkhalango ndi mitengo zathera ndi kulephera kupeza njira zoyenera zophikira.

MUTU 3
CHISANKHO CHAPATATU CHA 2019
3.1 Kuyambanso Mwatsopano
M’nthawi ino ya ufulu wademokalase, anthu m’dziko ali ndi udindo wosankha atsogoleri amene amawakhulupirira kuti adzakwaniritsa malonjezo ao amene adachita pa kampeni kapena anthu amene adaonetsapo kale kuti ali ndi kuthekera kokwaniritsa malonjezo ao. M’nthawi ino, Papa Fransisko akutikumbutsa kuti, “tizisankha atsogoleri osati potengera kuti amatipatsa ndalama kapena zinthu zina ndiponso osatengera zomwe amangobwebwetabwetabweta chabe, ai, koma anthu amene ali ndi mtima ndi luntha lotha kutsogolera anthu ndi kuwafikitsa kumene adalinga” (Addressing the fifth national conversion of the Italian Church, November 10, 2015).
Chaka chilichonse chachisankho chimapatsa anthu mwai wolowetsa m’Boma anthu amene amafunira zabwino dziko lao.
3.2 Makhalidwe Ofunikira a Anthu Ofuna Kuima Nawo Pa Chisankho
M’Kalata ino, monganso tidaafotokozera m’Kalata yathu ya 2013 yotchedwa (Kulimbikitsa Masomphenya a Tsogolo Lathu, mutu 4) panonso talemba mndandanda wa makhalidwe oyenereza anthu ofuna kuima nawo pa masankho kuti akhale pa maudindo.
• Kukhulupirika – tisankhe munthu amene anthu angamudalire chifukwa amalankhula zoona, amene amachita zomwe walankhula ndi kulonjeza, amene amavomereza momwe wayendetsera zinthu ndipo amalola kuti afufuzidwe m’mene adagwiritsira ntchito ndalama za dziko;
• Utsogoleri Wosintha Zinthu – tisankhe atsogoleri amene adzayesetsa kugwira ntchito ndi anzao pofuna kusintha mchitidwe wandale zachikale zomwe zimachedwetsa chitukuko m’dziko ndipo adzayesetsa kupereka mwai woti anthu ambiri m’dziko atukuke;
• Wosadzikonda – tisankhe munthu amene amakhudzidwa ndi zosowa za anthu ena m’dziko kuposa zofuna zake;
• Mtsogoleri Wotumikira – “Aliyense amene afuna kukhala wamkulu pakati panu ayenera kukhala mtumiki, ndipo aliyense amene akufuna kukhala woyambirira, ayenera kukhala kapolo wa onse. Chifukwa ngakhale Mwana wa Munthu sanabwere kuti ena amtumikire koma kuti Iye atumikire ena, ndi kupereka moyo wake chifukwa cha anthu ambiri” (Marko 10: 44).
• Mtsogoleri Wokhwima M’maganizo – tisankhe munthu amene angathe kumanga mfundo zoyenera ndi zothandiza mopanda mantha;
• Wolemekeza Malamulo – tisankhe munthu amene adzasunga ndi kutsata malamulo m’dziko;
• Wokonzeka Kutula Pansi Udindo – tisankhe munthu amene sadzakakamira kukhala pa udindo pamene nthawi yake yatha.
“Choncho inunso, mutachita zonse zimene adakulamulani, muziti; ‘ndife antchito chabe osayenera kulandira kanthu. Tangochita zimene tinayenera kuchita” (Luka 17: 10);
• Wosatsogoza Mtundu, Chigawo Kapena Chipani Chandale – dziko la Malawi likusowa kukhala ndi atsogoleri amene ali ndi chidwi ndi mfundo zosangoganizira mtundu kapena chigawo chimene akuchokera koma akhale atsogoleri ofunira zabwino za munthu aliyense m’dziko lao;
• Woopa Mulungu – popeza kuti Malawi ndi dziko loopa Mulungu, lisowa kukhala ndi atsogoleri oopa Mulungu moona, olemekeza ulemelero wa munthu ndinso osunga bwino mfundo za chikhulupiriro.
3.3 Kufunika Koti Amalawi Tonse Tisinthe Kaganizidwe
Titha kunena kuti, Amalawi amakondwera ndi ufulu wademokalase umene adaupeza. Komabe, kawirikawiri, amadandaula ndi kuloza chala atsogoleri chifukwa cha kusokonezeka kwa zinthu ndi chitukuko pakati pathu ndiponso chifukwa cha katangale ndi kuponderezana. Nthawi yakwana yoti ife Amalawi tidzifunse ndi kusinkhasinkha mozama momwe ife ngati nzika za dziko lino tathandizira pakuwonga zinthu zomwe ife timazidandaula, kuwiringula ndi kukhumudwa nazo. Ife Amalawi tikuyeneradi kusintha kaonedwe ndi kaganizidwe kathu ngati tifuna kuti dziko lathu, lomwe nthawi zambiri timalidandaula, lisinthedi. Pobwereza mau a Papa Fransisko, munthu aliyense payekhapayekha ali ndi kuthekera “kochita chisankho cha momwe angakonzere moyo ndi tsogolo lake kuti akwaniritse masomphenya ake” (Addressing the fifth national conversion of the Italian Church, November 10, 2015). M’munsimu muli maganizo othandiza a momwe tingasinthire kaonedwe ndi kaganizidwe kathu ngati Amalawi kuti tithe kuyambanso moyo watsopano:
• Utsogoleri wakatangale umalimbikitsidwa ndi kukakamiridwa ndi anthu odzikonda amene amapindula ndi utsogoleri wamtunduwo. Zili ndi ife nzika za m’dziko lino osati atsogoleri okha, kusiya kuthandizira ulamuliro wakatangale umene umalimbikitsidwa ndi mchitidwe wopereka ndi wongofuna kulandira zinthu – (handouts);
• Tiyeni aliyense mwa ife atenge udindo pofuna kukometsa moyo wake ndi kupewa kaganizidwe koti palibe chimene tingachite mwatokha chotha kutithandiza;
• Ngati nzika, tipewe kumangoyang’ana ku Boma ndi kwa atsogoleri andale kuti ndi amene angathetse mavuto athu. Chifukwatu mavuto ena amene Amalawi timakumana nawo ndi okhudza ifeyo ngati anthu patokhapatokha ndipo sasowa kuti boma kapena atsogoleri andale atithandize;
• Tiyeni Amalawi tidzavote mwanzeru povotera atsogoleri omwe ali okonzeka kutumikira osati kusankha atsogoleri pongotsata chipani chotchuka m’dera lathu.
Kusintha kwa kaganidwe kathu kotereku kangathandize kuti m’Boma mulowe atsogoleri amene angathe kuthetsa mavuto ndi zokhoma zimene dziko lathu lakumana nazo monga katangale, makhalidwe onyada, kukondera, kuopseza atolankhani, kusavomera kudzudzulidwa, kusadziwa chochita, kusakhudzidwa ndi mavuto a anthu omwe amadza chifukwa cha umphawi ndi kuwongonongeka kwa chilengedwe, kusakwaniritsa malonjezo, kusayenda bwino kwa chuma cha dziko ndi kusachita kalondolondo pa kagwiritsidwe ntchito ka ndalama.
Mau Otsiriza
Tikupempha Amalawi onse kuti athandize kudzetsa moyo watsopano m’dziko lathu lino, momwe choonadi, chilungamo ndi kulemekeza ulemerero wa munthu zidzakhale njira yathu ya moyo pakati pathu. Izi zikutanthauza kuti ife ngati nzika tisinthe kaganizidwe kathu ndipo mwapadera, iwonso amene tidzawasankhe adzasinthe kayendetsedwe ka Boma. Izinsotu zikutanthauza kuti tidzasankhe mwanzeru atsogoleri okonzeka kutumikira omwe angadzasanduke ngwazi (heros) zodzetsa kusintha ndi moyo watsopano. Atsogoleri otere adzakhala ngwazi osati chifukwa cha ntchito zao zabwino zokha ai, koma chifukwa chakuti adzaima ndi kumanga mfundo zao pa choonadi angakhale pamene ena sakugwirizana nao. Iwowa adzatchuka chifukwa chokana kupeputsa mfundo za ufulu wademokalase ngakhale apanikizidwe motani. Adzakhala oganizira nzika zonse m’dziko mosayang’anira zipani zomwe akuchokera. Adzatsata uphungu wonga wa Mose umene adalangiza atsogoleri amene adawasankha wakuti: “Musakondere poweruza. Aliyense, munthu wamba kapena wamkulu, mumuweruze chimodzimodzi. Musaopa wina aliyense, chifukwa chiweruzo chonse ndi cha Mulungu (Deuteronomo 1: 17). Monga Ambuye Yesu ndi Aneneri ena m’Chipangano Chakale, anthu amene amasanduka ngwazi pakati pa anthu, amakhala ndi adani ambiri ndipo mwinanso amataya miyoyo yao. Nthawi zina amuna ndi akazi angathe kutseka makutu ao ku choona ndipo mwina angathe kufika pa mlingo wopha munthu wonena choonayo. Koma tisaiwale kuti potsiriza, choona chimaululika. Ngwazi zimachita zinthu molimba mtima chifukwa zimakhulupirira kuti zomwe zikuchitazo ndi zolondola. Kuimira choona ndi chilungamo kumasowa kulimba mtima kwa tonsefe. Komatu iyi, ndi njira yokhayo yomwe tingadzetsere kusintha zinthu kuno ku Malawi.
Tikupempha Akatolika onse ndi anthu ena akufuna kwabwino kuti apitirize kukambirana mfundo zomwe zalembedwa m’kalata ino monga m’mabanja, m’miphakati kaya titi m’malimana, m’mabungwe a church konsolo, parish konsolo, m’sukulu zosiyanasiyana, m’zipatala, m’nyumba zofalitsa nkhani, m’magulu a Chilungamo ndi Mtendere, CADECOM, m’mabungwe a Akhristu Eniake, m’Zipani Zamumpingo, ndipo makamaka m’magulu a Achinyamata ndinso m’misonkhano yosiyanasiyana m’Madayosizi.
Amai Maria, Mai wa Ambuye athu Yesu Khristu, ndi chitsanzo chathu cha utumiki, atipempherere ife ndi dziko lathu kuti dziko la Malawi likondwerere ufulu weniweni wademokalase, ulamuliro wabwino ndi chitukuko cha munthu aliyense.
Most Reverend Thomas Msusa Chairman and Archbishop of Blantyre
Right Reverend Martin Mtumbuka Vice-Chairman and Bishop of Karonga
Most Reverend Tarsizio G. Ziyaye Archbishop of Lilongwe
Right Reverend Peter Musikuwa Bishop of Chikwawa
Right Reverend Montfort Stima Bishop of Mangochi
Right Reverend George Tambala Bishop of Zomba
Right Reverend John A. Ryan Bishop of Mzuzu
Very Reverend John Chithonje Diocesan Administrator of Dedza
Yotsindikizidwa pa: 29 April, Lamulungu la 5 la Pasaka, m’chaka cha 2018.
PASTORAL LETTERS OF THE EPISCOPAL CONFERENCE OF MALAWI
1. How to Build a Happy Nation (1961)
2. Living Our Faith (1992)
3. Choosing Our Future (1993)
4. Building Our Future (1994)
5. Let Us Care for Our Families (1994)
6. Families Take Care (World AIDS Day Message, 1994)
7. Let Us Care for the Orphans (World AIDS Day Message, 1995)
8. Pastoral Directives on Christian Burial (1996)
9. Walking Together in Faith (1996)
10. Come Back to Me and Live (1998)
11. Walking Together (1998)
12. Walking Together in Faith, Hope and Love (1999)
13. Deeping Our Christian Life (2000)
14. Celebrating the Centenary (2001)
15. Rejoicing and Vigilantly Living in Hope (2002)
16. Choosing Our Leaders in the Forthcoming Elections (2003)
17. The Body of Christ: Food and Light on Our Spiritual Journey (2004)
18. Renewing Our Lives and Society with the Power of the Holy Spirit (2006)
19. Taking Responsibility for Our Future: Together Towards the 2009 Elections (2008)
20. Celebrating the Year for Priests through a renewed commitment to Christ and His Church (2010)
21. Reading the Signs of the Times (2010)
22. Catholic Teaching on Homosexuality, Abortion, Population and Birth Control (2013)
23. Strengthening the Vision of our Destiny (2013)
24. Mercy of God as a Path of Hope (2016)

Bungwe la Aepiskopi Achikatolika M’malawi (ECM)

Sem comentários: